BUNGWE LA UZIMU (#13453)

*Pamene mulowa mchipinda chokumanira, nenani pemphero ili ndi mtima wogunda ndi chikondi cha Mulungu ndi lirime loyeretsedwa kuzonse koma chikumbukiro Chake, kuti Wamphamvu Zonseyo mwachifundo Akuthandizeni kupeza chipambano chachikulu:  
 O Mulungu, Mulungu wanga! Ife tili antchito Anu amene tatembenukira modzipereka kunkhope Yanu yoyera, amene tadzilekanitsa tokha kuzinthu zonse kupatula Inu pa Tsiku loyera-yerali. Ife tasonkhana mu 
Bungwe la Uzimu ili, wogwirizana m’malingaliro athu ndi m’maganizo athu, ndi mzolinga zathu zobvomerezana kukweza Mau Anu pakati pa anthu. O Ambuye, Mulungu wathu! Tipangeni ife kukhala zizindikiro za Chitsogozo Chanu choyera, mbendera za Chikhulupiliro Chanu chokwezeka pakati pa anthu, antchito kuchipangano 
Chanu champhamvu, O Inu Ambuye wathu wam’mwambamwamba, abvumbulutsi a umodzi Wanu Woyera mu ufumu Wanu wa Abha, ndi nyenyezi zowala zowunikira maiko onse. 
Ambuye! Tithandizeni ife kuti tikhale nyanja zoyendetsedwa ndi mafunde a chisomo Chanu chodabwitsa, mitsinje yoyenda kuchokera kumitundu Yanu yoyera-yera, zipatso zabwino pa mtengo wa chiphunzitso Chanu cha kumwamba, mitengo yogwedezedwa ndi mphepo ya Chaulere Chanu m’munda Wanu wakumwamba. O Mulungu! Pangani mizimu yathu kutsamira pa malemba a Umodzi Wanu woyera, mitima yathu kukondweretsedwa ndi m’bvumbi wa chisomo Chanu, kuti tigwirizane ngati mafunde a m’nyanja imodzi ndikulumikizana ngati Malawi akuwala Kwanu kwakukulu; kuti maganizo athu, malingaliro athu, kumva kwathu kukhale ngati choona chimodzi, kusonyeza mzimu wa umodzi kubzolera mdziko lonse lapansi. Ndinu wa Chisomo, wa Chaulere, Wopatsa, wa Mphamvu Zonse, wa Chifundo, Wachisoni.

-`Abdu'l-Bahá
-----------------------

BUNGWE LA UZIMU (#13454)

*Pemphero lonenedwa potseka msonkhano wa Bungwe Lauzimu.  
 O Mulungu! O Mulungu! Kuchokera ku ufumu wosaoneka wa umodzi Wanu tioneni ife tasonkhana mu msokhano wa uzimuwu, kukhulupirira mwa Inu, kukhulupirira zizindikiro Zanu, wolimba mu Pangano ndi Mawu Anu, okopedwa kwa Inu, tiyatseni ife ndi moto wa chikondi Chanu ndi kukhukupirika ku Chipembedzo Chanu.  
Ndife antchito m'munda Wanu, ofalitsa Chipembedzo Chanu, okhulupirika okupembedzani Inu, odzichepetsa kwa okondedwa Anu, odzitsitsa pa chitseko Chanu, ndipo tikukupemphani Inu kutilimbikitsa ife potumikira osankhika Anu, kutithandiza ife ndi makamu Anu osaoneka, kutilimbikitsa ife mukutumikira ndi kutipanga ife odzipereka ndi okonda kuyankhula ndi Inu.  
O Ambuye athu! Ndife ofooka, ndipo Inu ndi Wamphamvu, Wanyonga. Ndife opanda moyo, ndipo Inu Mzimu wopereka moyo, Ndife osowa, ndipo Inu ndi Wokwaniritsidwa, Wamphamvu.  
O Ambuye athu! Tembenuzirani nkhope zathu ku Chifundo Chanu, tidyetseni ife kuchokera ku gome la Kumwamba Kwanu ndi Chisomo Chanu chosefukira, tithandizeni ife ndi makamu a angelo Anu ndi kutilimbikitsa ife kupyolera mwa oyera a mu Ufumu wa Abhá.  
Indetu, Inu Ndinu Wopatsa, Wachifundo. Inu Ndinu Mwini wa Mphatso zonse, ndipo, indetu, Inu Ndinu Wachisoni ndi wa Chisomo.

-`Abdu'l-Bahá
-----------------------

